20 Choncho Davide anadzuka m’mawa kwambiri, atasiya nkhosa zake m’manja mwa wozisamalira. Iye ananyamula katundu wake ndi kunyamuka monga mmene Jese, bambo ake, anamuuzira.+ Atafika mkati mwa mpanda wa msasa,+ anapeza asilikali akupita kumalo omenyera nkhondo,+ akufuula mfuwu ya nkhondo.