Yesaya 20:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Iwo adzachita mantha ndiponso manyazi chifukwa chakuti anali kudalira Itiyopiya+ komanso chifukwa chakuti anali kusirira kukongola kwa Iguputo.+ Yesaya 31:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi. Ezekieli 30:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+
5 Iwo adzachita mantha ndiponso manyazi chifukwa chakuti anali kudalira Itiyopiya+ komanso chifukwa chakuti anali kusirira kukongola kwa Iguputo.+
3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi.
18 Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+