12 Dziko la Iguputo ndidzalisandutsa bwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu.+ Kwa zaka 40, mizinda yake idzakhala mabwinja pakati pa mizinda yopanda anthu.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira m’mayiko ena.”+
18 “Iwe mwana wa munthu, lirira khamu la ku Iguputo ndi kulengeza kuti lidzatsikira kumanda.+ Dzikolo ndi anthu a mitundu yamphamvu adzatsikira pansi pa nthaka+ limodzi ndi amene akutsikira kudzenje.+