Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzapezerapo ulemerero mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi momwemo.

  • 2 Mafumu 19:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+

  • Salimo 83:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

      Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

  • Salimo 148:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Iye adzakweza nyanga* ya anthu ake.+

      Adzachititsa kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,+

      Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.+

      Tamandani Ya, anthu inu!+

  • Ezekieli 36:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

  • Ezekieli 39:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “‘Ndidzasonyeza ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu. Mitundu yonse ya anthu idzaona chiweruzo chimene ndidzapereke+ ndiponso mphamvu za dzanja langa.+

  • Mateyu 6:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Koma inu muzipemphera motere:+

      “‘Atate wathu wakumwamba, dzina+ lanu liyeretsedwe.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena