3 Tsopano ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi+ pamene unali, ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Kenako Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu wovala zovala zansalu uja,+ yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera.