Yesaya 6:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Aliyense anali kuuza mnzake kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.+ Zonse zimene zili padziko lapansi zimasonyeza ulemerero wake.” Ezekieli 3:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Chotero ndinanyamuka n’kupita kuchigwako. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova waimirira,+ ngati ulemerero umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Ezekieli 10:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo.
3 Aliyense anali kuuza mnzake kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.+ Zonse zimene zili padziko lapansi zimasonyeza ulemerero wake.”
23 Chotero ndinanyamuka n’kupita kuchigwako. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova waimirira,+ ngati ulemerero umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+
4 Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo.