34 Koma ansembe+ anali ochepa kwambiri ndipo sanathe kusenda nyama zonse za nsembe zopsereza.+ Choncho abale awo+ Alevi anawathandiza mpaka ntchitoyo inatha+ ndiponso kufikira pamene ansembewo anadziyeretsa,+ popeza Alevi ankafunitsitsa kudziyeretsa kuposa ansembe.+