Ezara 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+ Yesaya 1:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova wa makamu akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,+ tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.+ Yesaya 37:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ Ezekieli 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+
15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+
9 Yehova wa makamu akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,+ tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.+
31 Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+
8 “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+