Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 30:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+

  • Yeremiya 44:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Anthu amene adzathawa lupanga kuchoka ku Iguputo kubwerera kudziko la Yuda adzakhala ochepa.+ Ndipo otsala onse ochokera ku Yuda amene akubwera m’dziko la Iguputo kuti adzakhalemo monga alendo adzadziwa kuti ndi mawu a ndani amene ali oona, mawu anga kapena mawu awo.”’”+

  • Ezekieli 14:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Koma ndithu m’dzikolo mudzatsala kagulu ka anthu amene adzapulumuke ndipo adzatulutsidwamo.+ Taonani ana aamuna ndi aakazi! Iwo akubwera kwa inu, ndipo mudzaona njira yawo ndi zochita zawo.+ Inu mudzatonthozedwa pambuyo pa tsoka limene ndidzabweretse pa Yerusalemu, ngakhalenso pambuyo pa zonse zimene ndidzabweretsere mzindawo.’”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena