Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuiwala pangano+ la makolo anu limene anawalumbirira.

  • 2 Mbiri 36:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Kuwonjezera apo, Nebukadinezara anagwira anthu amene sanaphedwe ndi lupanga ndipo anawatenga kupita nawo ku Babulo.+ Anthuwo anakakhala antchito+ ake ndi a ana ake kufikira pamene ufumu wa Perisiya+ unayamba kulamulira.

  • Yesaya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 M’dzikolo mudzakhalabe chakhumi+ ndipo chidzakhalanso chinthu chofunika kuchitentha ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa+ pamatsala chitsa.+ Mbewu yopatulika idzakhala chitsa chake.”+

  • Yesaya 10:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+

  • Ezekieli 6:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+

  • Mika 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Otsala a Yakobo,+ pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzakhala ngati mame ochokera kwa Yehova.+ Iwo adzakhala ngati mvula yamvumbi imene ikuwaza pazomera,+ yomwe sidalira munthu kapena kuyembekezera ana a anthu ochokera kufumbi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena