Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+

  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • 2 Mbiri 30:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mukabwerera+ kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo+ ndi anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina. Chotero iwo adzaloledwa kubwerera kudziko lino+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo+ ndiponso wachifundo,+ ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwerera kwa iye.”+

  • Nehemiya 9:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Koma mwachifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya,+ pakuti inu ndinu Mulungu wachisomo+ ndi wachifundo.+

  • Salimo 86:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo,+

      Wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+

  • Yesaya 54:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Kwa kanthawi kochepa ndinakusiyiratu,+ koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+

  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+

  • 2 Akorinto 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Atamandike Mulungu ndi Atate+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu+ ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena