19 Ngati zingakukomereni mfumu,+ lamulani monga mfumu ndipo lamuloli alilembe m’malamulo+ a Perisiya ndi Mediya kuti zimene mwalamula zisasinthe.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke ulemu wake wachifumu kwa mkazi wina, mkazi wabwino kuposa iyeyu.