Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 1:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Pakuti anthu adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene inu munali kuilakalaka,+ ndipo mudzagwetsa nkhope zanu chifukwa cha minda imene mwasankha.+

  • Yesaya 57:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 amene mumadzutsa chilakolako chanu pakati pa mitengo ikuluikulu+ ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+ Kodi si inu amene mumapha ana m’zigwa* pakati pa matanthwe?+

  • Yeremiya 2:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “‘Ine ndinaphwanya goli lako kukhala zidutswazidutswa kalekale.+ Ndinadula zingwe zimene anakumanga nazo. Koma iwe unati: “Sindikutumikirani,” ndipo unagona motangadza+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ n’kumachita uhule+ pamenepo.

  • Ezekieli 20:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko+ limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali+ ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena