Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 2:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “‘Ine ndinaphwanya goli lako kukhala zidutswazidutswa kalekale.+ Ndinadula zingwe zimene anakumanga nazo. Koma iwe unati: “Sindikutumikirani,” ndipo unagona motangadza+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ n’kumachita uhule+ pamenepo.

  • Yeremiya 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Yehova anapitiriza kulankhula nane m’masiku a Mfumu Yosiya kuti:+ “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita?+ Akupita kuphiri lililonse lalitali+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ kuti akachite uhule kumeneko.+

  • Ezekieli 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+

  • Hoseya 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri+ ndipo amafukiza nsembe zautsi pazitunda.+ Amachitanso zimenezi pansi pa zimitengo zikuluzikulu, mitengo ya mlanje, ndi mitengo yaikulu, chifukwa ili ndi mthunzi wabwino.+ N’chifukwa chake ana anu aakazi amachita dama ndipo apongozi anu aakazi amachita chigololo.

  • Aroma 6:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kodi pa nthawiyo munali kukhala ndi zipatso zotani?+ Zinali zinthu+ zimene tsopano mumachita nazo manyazi. Ndipo pothera pake pa zinthu zimenezo ndi imfa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena