4 “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+
“‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.