6 Choncho iwo anasonkhana pamodzi ku Mizipa, ndipo anali kutunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova ndi kusala kudya tsiku limenelo.+ Ali kumeneko, anayamba kunena kuti: “Tachimwira Yehova.”+ Pamenepo, Samueli anayamba kuweruza+ ana a Isiraeli ku Mizipa.