Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 8:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Hazaeli ataona zimenezi anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira mbuyanga?” Elisa anayankha kuti: “Chifukwa ndikudziwa bwino zoipa+ zimene iweyo udzachitire ana a Isiraeli. Malo awo otetezedwa udzawatentha ndi moto, amuna ochita kusankhidwa pakati pawo udzawapha ndi lupanga, ana awo aang’ono udzawaphwanyaphwanya,+ ndipo akazi awo apakati udzawatumbula.”+

  • 2 Mafumu 10:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 M’masiku amenewo, Yehova anayamba kulanda dziko la Isiraeli pang’ono ndi pang’ono, ndipo Hazaeli+ anapitiriza kupha anthu m’madera onse a dziko la Isiraeli.

  • 2 Mafumu 10:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Anayambira ku Yorodano chakotulukira dzuwa, dziko lonse la Giliyadi,+ Agadi,+ Arubeni+ ndi Amanase,+ kuyambira ku Aroweli+ yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni, ngakhalenso Giliyadi ndi Basana.+

  • 2 Mafumu 13:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Yehoahazi sanatsale ndi anthu alionse kupatulapo amuna 50 okwera pamahatchi, magaleta 10, ndi asilikali 10,000 oyenda pansi,+ chifukwa mfumu ya Siriya inawawononga+ ndi kuwapondaponda ngati fumbi la popunthira mbewu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena