Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 “Matemberero onsewa+ adzakugwera, kukutsatira ndi kukupeza kufikira utafafanizika,+ chifukwa sunamvere mawu a Yehova Mulungu wako mwa kusunga malamulo ndi mfundo zake zimene anakupatsa.+

  • Deuteronomo 28:63
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 63 “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+

  • 2 Mafumu 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Panali pa nthawi imeneyi pamene Menahemu anachoka ku Tiriza n’kupita kukaukira mzinda wa Tifisa, n’kupha anthu onse amene anali mmenemo. Anawononganso dera lozungulira mzindawo chifukwa anthu ake sanamutsegulire chipata, ndipo akazi onse apakati a mumzindawo anawatumbula.+

  • Hoseya 10:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa,+ ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena