Deuteronomo 30:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ Salimo 103:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+ Danieli 9:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo+ ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+ Hoseya 2:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.*+ Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo, komanso chifukwa cha kukoma mtima kwanga kosatha ndi chifundo changa.+ Aefeso 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka,+ mwachikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,+
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+
19 Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.*+ Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo, komanso chifukwa cha kukoma mtima kwanga kosatha ndi chifundo changa.+
4 Koma Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka,+ mwachikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,+