23 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika.+ Kupereka zinthu zimenezi n’kofunikadi, koma osanyalanyaza zinthu zinazo.