39 Pakuti ana a Isiraeli ndi ana a Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta kuzipinda zodyera. Kumeneku ndi kumene kuli ziwiya za kumalo opatulika ndi ansembe amene anali kutumikira,+ olondera pazipata+ ndi oimba,+ ndipo tisanyalanyaze nyumba ya Mulungu wathu.+