8 “‘Tamvera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi pamaso pako, pakuti iwo ndi amuna amene ali ngati zizindikiro zolosera zam’tsogolo.+ Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+
11 Pa choperekacho ukatengepo siliva ndi golide n’kupangira chisoti chachifumu chaulemerero.+ Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki.