25 Ayuda+ ndi Aisiraeli anapitiriza kukhala mwabata.+ Aliyense anali pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+ kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ masiku onse a Solomo.
16 Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Ndigonjereni,+ ndipo bwerani kwa ine. Aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu,+ komanso aliyense azimwa madzi a m’chitsime chake,+
4 Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu+ ndipo sipadzakhala wowaopsa,+ pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.+