15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa+ pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.+
9 Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwa+ ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati+ wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: “Awa ndi mawu oona a Mulungu.”+