Mateyu 26:73 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera ndi kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.”+ Luka 22:59 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 59 Patapita pafupifupi ola lathunthu, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, ndipo iyeyu ndi Mgalileya!”+ Yohane 18:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?”
73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera ndi kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.”+
59 Patapita pafupifupi ola lathunthu, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, ndipo iyeyu ndi Mgalileya!”+
26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?”