Yesaya 66:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Zinthu zonsezi ndinazipanga ndi dzanja langa, choncho zinakhalapo,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzayang’ana munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima,+ ndiponso wonjenjemera ndi mawu anga.+ Ezekieli 7:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Anthu awo opulumuka adzathawa+ ndipo adzakhala pamapiri ngati njiwa za m’zigwa,+ aliyense akulira chifukwa cha zolakwa zake. 1 Akorinto 10:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 N’chifukwa chake amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.+ 2 Akorinto 7:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+
2 “Zinthu zonsezi ndinazipanga ndi dzanja langa, choncho zinakhalapo,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzayang’ana munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima,+ ndiponso wonjenjemera ndi mawu anga.+
16 Anthu awo opulumuka adzathawa+ ndipo adzakhala pamapiri ngati njiwa za m’zigwa,+ aliyense akulira chifukwa cha zolakwa zake.
10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+