Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 4:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pitirizani kutambasula dzanja lanu ndi kupereka machiritso, komanso kuti zizindikiro ndi zodabwitsa+ zipitirize kuchitika m’dzina+ la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+

  • Machitidwe 6:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Tsopano Sitefano, anali wodzazidwa ndi chisomo komanso mphamvu, ndipo anali kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu+ pakati pa anthu.

  • Machitidwe 7:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Munthu ameneyo anawatsogolera ndi kutuluka nawo,+ atachita zodabwitsa ndi zizindikiro mu Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndi m’chipululu kwa zaka 40.+

  • Machitidwe 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chotero kwa nthawi yaitali, anakhala akulankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova. Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, mwa kulola kuti zizindikiro ndi zodabwitsa zichitike kudzera mwa ophunzirawo.+

  • Machitidwe 15:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pamenepo gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera Baranaba ndi Paulo pamene anali kufotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo pakati pa anthu a mitundu ina.+

  • Aroma 15:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 ndiponso pogwiritsa ntchito mphamvu yochita zizindikiro ndi zinthu zodabwitsa zolosera zam’tsogolo,+ mwa mphamvu ya mzimu woyera. Chotero ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu+ kuyambira ku Yerusalemu, kuzungulira+ mpaka ku Iluriko.

  • 2 Akorinto 12:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndithudi inuyo munaona umboni wakuti ndine mtumwi,+ poona mmene ndinapiririra,+ komanso poona zizindikiro, zodabwitsa, ndi ntchito zamphamvu zimene ndinachita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena