2 Ngakhale kuti panopa ndili kutali ndi inu, koma muone mawu angawa ngati kuti ndili limodzi nanu kachiwiri. Choncho, monga mmene ndinachitira kale, ndikuchenjeza anthu amene anachimwa, komanso ena onse, kuti ndikadzabweranso kumeneko sindidzalekerera munthu.+