36 Koma ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane, pakuti ntchito zenizenizo zimene Atate wanga anandipatsa kuti ndizikwaniritse, ntchito zimene ine ndikuchita,+ zikundichitira umboni kuti Atate ananditumadi.
38 Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo,+ kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”+