Yohane
10 “Ndithudi ndikukuuzani, Wolowa m’khola la nkhosa mochita kukwera pamalo ena osati kudzera pakhomo,+ ameneyo ndi wakuba ndiponso wofunkha.+ 2 Koma wolowera pakhomo,+ ameneyo ndiye m’busa+ wa nkhosazo.+ 3 Mlonda wa pakhomo+ amamutsegulira ameneyu, ndipo nkhosa+ zimamvera mawu ake. Nkhosa zakezo amazitchula mayina ndi kuzitsogolera kutuluka nazo. 4 Akatulutsa zake zonse kunja, amazitsogolera, ndipo nkhosazo zimamutsatira,+ chifukwa zimadziwa mawu ake.+ 5 Mlendo sizidzamutsatira ayi koma zidzamuthawa,+ chifukwa sizidziwa mawu a alendo.”+ 6 Yesu ananena fanizoli kwa iwo, koma iwo sanadziwe tanthauzo la zinthu zimene anali kuwauzazo.+
7 Choncho Yesu anawauzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ine ndine khomo+ la nkhosa. 8 Onse amene abwera m’malo mwa ine ndi akuba ndiponso ofunkha,+ ndipo nkhosa sizinawamvere.+ 9 Ine ndine khomo.+ Aliyense wolowa kudzera mwa ine adzapulumuka, ndipo azidzalowa ndi kutuluka, kukapeza msipu.+ 10 Wakuba+ sabwera ndi cholinga china ayi, koma kudzaba, kudzapha ndi kudzawononga.+ Koma ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka. 11 Ine ndine m’busa wabwino.+ M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.+ 12 Munthu waganyu,+ amene si m’busa ndipo nkhosazo si zake, akaona mmbulu ukubwera amasiya nkhosazo ndi kuthawa, pamenepo mmbuluwo umazigwira ndi kuzibalalitsa,+ 13 chifukwa iye ndi waganyu+ chabe, ndipo sasamala za nkhosazo.+ 14 Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa,+ izonso zimandidziwa,+ 15 monga mmene zilili kuti Atate amandidziwa, inenso ndimawadziwa Atate.+ Chotero, ndipereka moyo wanga chifukwa cha nkhosazo.+
16 “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+ 17 Chimene Atate amandikondera n’chakuti,+ ndikupereka moyo wanga+ kuti ndikaulandirenso. 18 Palibe munthu amene akuuchotsa kwa ine, koma ndikuupereka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupereka, ndiponso ndili ndi mphamvu zoulandiranso.+ Atate wanga ndi amene anandilamula+ kuchita zimenezi.”
19 Apanso panakhala kugawanika+ maganizo pakati pa Ayuda chifukwa cha mawu amenewa. 20 Ambiri a iwo anali kunena kuti: “Ameneyu ali ndi chiwanda+ ndipo ndi wamisala. N’chifukwa chiyani mukumumvetsera?” 21 Ena anali kunena kuti: “Amenewa si mawu a munthu wogwidwa ndi chiwanda ayi. Kodi chiwanda chingatsegule maso a anthu akhungu?”
22 Pa nthawiyo mu Yerusalemu munachitika chikondwerero cha kupereka kachisi kwa Mulungu. Inali nyengo ya chisanu, 23 ndipo Yesu anali kuyenda m’kachisimo, m’khonde la zipilala la Solomo.+ 24 Choncho Ayuda anamuzungulira ndi kuyamba kumuuza kuti: “Utivutitsa maganizo mpaka liti? Ngati ndiwedi Khristu,+ tiuze mosapita m’mbali.”+ 25 Yesu anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simukukhulupirira. Ntchito zimene ine ndikuchita m’dzina la Atate wanga, zikundichitira umboni.+ 26 Koma inu simukukhulupirira, chifukwa si inu nkhosa zanga.+ 27 Nkhosa+ zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa, ndipo izo zimanditsatira.+ 28 Ndidzazipatsa moyo wosatha,+ moti sizidzawonongeka,+ komanso palibe amene adzazitsomphole m’dzanja langa.+ 29 Chimene Atate+ wanga wandipatsa n’chofunika kuposa zinthu zonse,+ ndipo palibe amene angazitsomphole m’dzanja la Atate.+ 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”+
31 Apanso Ayudawo anatola miyala kuti amugende.+ 32 Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Tsopano mukundiponya miyala chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?” 33 Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ayi, koma chifukwa chonyoza Mulungu.+ Iwe ndiwe munthu wamba koma ukudziyesa mulungu.”+ 34 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo chanu sanalembemo+ kuti, ‘Ine ndinati: “Inu ndinu milungu”’?+ 35 Ngati anthu amene anatsutsidwa ndi mawu a Mulungu anawatcha ‘milungu,’+ ndipo Malemba satha mphamvu,+ 36 nanga kodi inu mukundiuza ine woyeretsedwa ndi Atate ndi kutumizidwa m’dziko kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ chifukwa ndanena kuti, Ndine Mwana wa Mulungu?+ 37 Ngati sindikuchita ntchito+ za Atate wanga, musandikhulupirire. 38 Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo,+ kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”+ 39 Pamenepo anayesanso kumugwira,+ koma anawazemba.+
40 Chotero anawolokanso Yorodano ndi kupita kumene Yohane anali kubatizira+ poyamba, ndipo anakhala kumeneko. 41 Anthu ambiri anabwera kwa iye, ndi kuyamba kunena kuti: “Yohane sanachite chizindikiro chilichonse, koma zonse zimene Yohane ananena zokhudza munthu uyu zinali zoona.”+ 42 Choncho anthu ambiri kumeneko anamukhulupirira.+