-
Deuteronomo 30:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 [Ngati udzamvera malamulo a Yehova Mulungu wako,] amene ndikukupatsa lero ndi kukonda Yehova Mulungu wako,+ kuyenda m’njira zake ndi kusunga malamulo ake,+ mfundo zake ndi zigamulo zake,+ pamenepo udzakhaladi ndi moyo+ ndi kuchulukana. Ndipo Yehova Mulungu wako adzakudalitsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+
-
-
Nehemiya 9:29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+
-