4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+
29 Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+
11 Popeza muli naye pa ubwenzi,+ mwadulidwa,+ osati ndi manja a anthu koma mwa kuvula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero.