Miyambo 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+ Luka 17:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Samalani ndithu. Ngati m’bale wako wachita tchimo um’dzudzule,+ ndipo akalapa umukhululukire.+ Agalatiya 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+ Tito 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+ 1 Petulo 3:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+
2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+
15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.