Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 61:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+ pakuti Yehova wandidzoza+ kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+ Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima,+ ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndiponso ndikatsegule maso a akaidi.+

  • Luka 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Pamenepo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba, akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”+

  • Luka 4:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+

  • Machitidwe 4:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode,* Pontiyo Pilato,+ pamodzi ndi anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzinda uno ndi kuukira Yesu, mtumiki wanu woyera,+ amene inu munamudzoza.+

  • Machitidwe 10:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, kuti Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye,+ anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena