18 “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+
18 Ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mu mdima+ ndi kuwatembenuzira ku kuwala.+ Kuwachotsa m’manja mwa Satana+ ndi kuwatembenuzira kwa Mulungu, kuti machimo awo akhululukidwe+ ndi kukalandira cholowa+ pamodzi ndi oyeretsedwa,+ mwa chikhulupiriro chawo mwa ine.’