6“Bwerani anthu inu. Tiyeni tibwerere kwa Yehova,+ pakuti iye watikhadzulakhadzula+ koma adzatichiritsa.+ Wakhala akutivulaza koma adzamanga zilonda zathu.+
14 “Ine ndidzawawombola ku Manda*+ ndiponso ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?+ Koma Efuraimu sindimumverabe chisoni.+