4 Koma ngati mkazi wamasiye aliyense ali ndi ana kapena adzukulu, amenewo aphunzire kukhala odzipereka kwa Mulungu m’banja mwawo choyamba,+ mwa kubwezera kwa makolo+ ndi agogo awo zowayenerera, pakuti zimenezi zimakondweretsa Mulungu.+
27 Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+