Afilipi 2:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Chotero, okondedwa anga, monga mmene mwakhalira omvera nthawi zonse,+ osati pokhapokha ine ndikakhalapo,* koma mofunitsitsa kwambiri tsopano pamene ine kulibe, pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha+ ndi kunjenjemera. 2 Timoteyo 2:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka+ pamaso pa Mulungu, wantchito+ wopanda chifukwa chochitira manyazi+ ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+ Aheberi 4:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+ Yuda 3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Okondedwa,+ ngakhale kuti ndinali kuyesetsa kuti ndikulembereni za chipulumutso chimene tonsefe tili nacho,+ ndaona kuti ndi bwino kuti ndikulembereni zokulimbikitsani kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro+ chomwe chinaperekedwa kamodzi kokha kwa oyerawo.+
12 Chotero, okondedwa anga, monga mmene mwakhalira omvera nthawi zonse,+ osati pokhapokha ine ndikakhalapo,* koma mofunitsitsa kwambiri tsopano pamene ine kulibe, pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha+ ndi kunjenjemera.
15 Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka+ pamaso pa Mulungu, wantchito+ wopanda chifukwa chochitira manyazi+ ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+
11 Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+
3 Okondedwa,+ ngakhale kuti ndinali kuyesetsa kuti ndikulembereni za chipulumutso chimene tonsefe tili nacho,+ ndaona kuti ndi bwino kuti ndikulembereni zokulimbikitsani kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro+ chomwe chinaperekedwa kamodzi kokha kwa oyerawo.+