Mateyu 24:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu+ ndi aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu+ ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.+ Machitidwe 20:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu+ yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. 2 Petulo 2:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Komabe, pakati pa anthuwo panadzakhala aneneri onyenga. Momwemonso padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.+ Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga ndipo adzakana ngakhale iye amene anawagula,+ n’kudzibweretsera chiwonongeko chofulumira. 1 Yohane 2:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto,+ ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera,+ ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri.+ Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. Chivumbulutso 2:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 ‘Ndikudziwa ntchito zako,+ khama lako, ndi kupirira kwako, ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Iwe unayesanso+ anthu amene amadzitcha atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama.
24 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu+ ndi aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu+ ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.+
29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu+ yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi.
2 Komabe, pakati pa anthuwo panadzakhala aneneri onyenga. Momwemonso padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.+ Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga ndipo adzakana ngakhale iye amene anawagula,+ n’kudzibweretsera chiwonongeko chofulumira.
18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto,+ ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera,+ ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri.+ Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto.
2 ‘Ndikudziwa ntchito zako,+ khama lako, ndi kupirira kwako, ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Iwe unayesanso+ anthu amene amadzitcha atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama.