4 Iwe udzafera m’mapiri a ku Isiraeli+ limodzi ndi magulu ako onse a asilikali ndi anthu a mitundu ina amene adzakhale nawe. Ndidzakuperekani kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.”’+
17 Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame+ zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,