Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 102:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Munakhazikitsa maziko a dziko lapansi kalekale,

      Ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu.+

  • Yesaya 42:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Mulungu woona Yehova,

      Amene analenga kumwamba ndiponso Mulungu Wamkulu amene anakutambasula,+

      Amene anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo,+

      Amene amapereka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo,+

      Komanso mzimu* kwa anthu amene amayenda padzikolo,+ wanena kuti:

  • Yesaya 45:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chifukwa Yehova,

      Mlengi wakumwamba,+ Mulungu woona,

      Amene anaumba dziko lapansi, amene analipanga ndi kulikhazikitsa mwamphamvu,+

      Amene sanalilenge popanda cholinga,* koma analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti:

      “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.

  • Aroma 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa,+ ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu wake,+ zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.

  • Aheberi 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Iye akunenanso kuti: “Ambuye, pachiyambipo munakhazikitsa maziko a dziko lapansi, ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu.

  • Chivumbulutso 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Ndinu woyenera, inu Yehova* Mulungu wathu kulandira ulemerero,+ ulemu+ ndi mphamvu+ chifukwa munalenga zinthu zonse+ ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”

  • Chivumbulutso 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye analumbira mʼdzina la Mulungu amene adzakhale ndi moyo mpaka kalekale,+ amene analenga kumwamba ndi zinthu zonse zimene zili kumeneko, dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo komanso nyanja ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo.+ Analumbira kuti: “Nthawi yodikira yatha.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena