-
Aheberi 8:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Utumiki umene amuna amenewa akuchita uli ngati chifaniziro ndiponso chithunzi+ cha zinthu zakumwamba.+ Izi zikufanana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa Mose atatsala pangʼono kumanga chihema. Lamulo lake linali lakuti: “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+
-
-
Aheberi 9:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anadzera mʼchihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti sichipezeka padzikoli.
-