-
Agalatiya 3:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndiye kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu? Ayi ndithu. Chifukwa pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo, bwenzi tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chotsatira chilamulo.
-
-
Aheberi 7:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kukhala ndi ansembe a fuko la Levi kunali mbali ya Chilamulo cha Mose chimene Aisiraeli anapatsidwa. Ndiye zikanakhala kuti ansembe a fuko la Levi angathandize anthu kukhala angwiro,+ kodi pakanafunikanso wansembe ngati Melekizedeki?+ Kodi sizikanakhala zokwanira kungokhala ndi wansembe ngati Aroni?
-