-
Akolose 2:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Choncho musalole kuti munthu aliyense akuweruzeni chifukwa cha chakudya ndi chakumwa+ kapena chikondwerero chinachake kapenanso kusunga tsiku limene mwezi watsopano waoneka+ kapena kusunga sabata.+ 17 Zinthu zimenezi ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera,+ koma zenizeni zake zinakwaniritsidwa ndi Khristu.+
-
-
Aheberi 8:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Utumiki umene amuna amenewa akuchita uli ngati chifaniziro ndiponso chithunzi+ cha zinthu zakumwamba.+ Izi zikufanana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa Mose atatsala pangʼono kumanga chihema. Lamulo lake linali lakuti: “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+
-