-
Ekisodo 29:15-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno utenge nkhosa imodzi, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 16 Nkhosayo uiphe nʼkutenga magazi ake ndipo uwawaze mbali zonse za guwa lansembelo.+ 17 Nkhosayo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake nʼkuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18 Nkhosa yonseyo uiwotche kuti utsi wake ukwere mʼmwamba kuchokera paguwalo. Imeneyo ndi nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.*+ Ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-
-
Levitiko 1:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa kuti iphimbe machimo ake.
-