-
Ekisodo 29:22-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndiyeno pankhosayo utengepo mafuta ndi mchira wa mafuta ndi mafuta okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake+ ndi mwendo wakumbuyo wakumanja, chifukwa nkhosayo ndi yowaikira kuti akhale ansembe.+ 23 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mkate wobulungira, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala. 24 Zonsezi uziike mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake, ndipo uziyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. 25 Kenako uzitenge mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza, kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-