-
Levitiko 14:53Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
53 Kenako aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo, kunja kwa mzinda. Akatero aziyeretsa nyumbayo, ndipo idzakhala yoyera.
-
-
Levitiko 16:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndipo Aroni aziika manja ake onse pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza zolakwa zonse za Aisiraeli ndiponso machimo awo onse. Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi+ ija nʼkuipereka kwa munthu amene amusankhiratu kuti akaisiye kuchipululu. 22 Mbuziyo izinyamula zolakwa zawo zonse+ pamutu pake ndipo aziitumiza kuchipululu.+
-
-
Yesaya 53:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Koma ifeyo tinkamuona ngati munthu amene wagwidwa ndi matenda, amene walangidwa* ndi Mulungu ndiponso kuzunzidwa.
-