-
Numeri 28:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse,* muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ 12 Pa ngʼombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wothira mafuta wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yake yambewu.+ Nkhosa yamphongo imodziyo muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta, wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yemwe ndi nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa,*+ nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.
-