-
2 Mbiri 2:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ine ndikumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga kuti ikhale yopatulika kwa iye. Ndikufuna kuti ndiziperekamo nsembe za mafuta onunkhira pamaso pake+ ndiponso kuti nthawi zonse muzikhala mkate wosanjikiza.*+ Ndiziperekamonso nsembe zopsereza mʼmawa ndi madzulo,+ pa Masabata,+ masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi pa nthawi ya zikondwerero+ za Yehova Mulungu wathu. Aisiraeli afunika azichita zimenezi mpaka kalekale.
-
-
Nehemiya 10:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Kuwonjezera pamenepo, tinalonjeza kuti chaka chilichonse aliyense azipereka ndalama zasiliva zolemera magalamu 4* kuti akazigwiritse ntchito pa utumiki wapanyumba* ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsenso ntchito pokonza mkate wosanjikiza,*+ nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse, nsembe yopsereza yoperekedwa nthawi zonse pa Masabata+ ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka,+ madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika, nsembe yamachimo+ yophimba machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu wathu.
-