-
Numeri 3:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema+ ndi nsalu yoyala pachihemacho, nsalu yake yophimba,+ nsalu yotchinga pakhomo,+ 26 nsalu+ za mpanda wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe za chinsalu chake, komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.
-
-
Numeri 4:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Anthu amʼmabanja a Agerisoni anapatsidwa ntchito yosamalira ndi kunyamula zinthu izi:+ 25 Azinyamula nsalu za chihema kapena kuti chihema chokumanako,+ nsalu yophimba chihema, chophimba cha chikopa cha katumbu chomwe chili pamwamba pake+ ndi nsalu yotchinga pakhomo la chihema chokumanako.+ 26 Azinyamulanso nsalu za mpanda wa bwalo,+ nsalu yotchinga khomo la mpanda+ umene wazungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zake zonse ndi zinthu zina zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumikiwu. Ntchito imene azigwira ndi imeneyi.
-